PAC yatsindika kufunika kwa mfundo zokhwima osati zozizira pokopa anthu


DPP Rally

Bungwe la atsogoleri a zipembedzo la Public Affairs Committee (PAC) lati pomwe nyengo yokopa anthu yayandikira, omwe akufuna kupikisana nawo pa mipando maka wa mtsogoleri wa dziko asataye nthawi ndi ntchedzera (jokes) koma awumbe mfundo zomwe zithandize osankha kupanga chiganizo.

Mneneli wa bungwe la PAC, Gilford Matonga wati atsogoleri asaononge dzikoli ndi ntchedzera komanso kulankhula zozizira koma alankhule mfundo zomwe zimange komanso kutukula dziko la Malawi.

A Matonga ati mfundo zabwino ndi zokhwima ziwathandiza ovota kuti apange chisankho chogwirika pomwe akupita kokasankha atsogoleri molingana ndi masomphenya ake.

Poyankhula ndi wayilesi zina mdziko muno, a Matonga atinso chisankho chomwe chikudza pa 16 September ndi chisankho chofunika, ndipo alimbikitsa kulorana kuti opikisana nawo athe kufika malo onse m’Malawi muno kukachita misonkhano yokopa anthu popanda chowaletsa ndipo mafumu akhale patsogolo kulankhula kwa anthu awo za ubwino wa umodzi ndi kulolerana.

“Chisankhochi nchofunika ndipo aliyense akhale ndi mpata oponda paliponse kukachita misonkhano yokopa anthu poti amene asankhidwe akhala mtsogoleri oyang’anira anthu onse,” analankhula a Matonga.

Bishop Matonga anatsindika kuti ziwawa sizikufunika mnyengoyi chifukwa zimakanikitsa kuti munthu amene anthu akumfuna apambane poti anthu amatsata mfundo, ndipo pasakhale malire poti yankho lili ndi ovota.

Naye olankhulapo pa nkhani za ndale ndi zochitika ndziko a Ceaser Kondowe ati pomwe nyengo yokopa anthu yanunkhira, atsogoleri ndi anthu omwe apewe kugwiritsa ntchito ndalama kukolezera zipolowe kutchingira ena kukopa anthu.

A Kondowe ati atsogoleri akuyenera akalankhule mfundo kwa anthu ndipo aMalawi iwo eni akhale ndi mpata kusiyanitsa.

Bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) litsekula nyengo yokopa anthu kuyambira pa 14 July mpaka pa 14 September chaka chino.

Mneneli wa bungweli Sangwani Mwafulirwa wati nyengoyi akayitsekulira, opikisana akhonza kuyamba kuthamanga ndi mfundo mwa mtendere kwa anthu.

Malinga ndi bungwe la MEC opikisana okwana khumi ndi asanu 15 ndi omwe atenga kale zikhalata kuti adzapikisana nawo pa masankho osakha mtsogoleri

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading