Kumasekelera munthu owononga kuti apitilile kuwononga ndi chimodzi chomwe chawononga dziko lino – Chakwera


Lazarus Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wati dziko la Malawi likuyenera kumangidwanso pa maziko a mphamvu ndipo kusekelera anthu owononga ndi zina zomwe zasakaza maziko a dziko lino.

Chakwera wati dziko la Malawi palibe chomwe lingaphule ngati lingamapitilire kutaya maziko a chikhalidwe posekelera anthu owononga omwe akhazikika pa kudya za ulele, kulalata, kunyoza, chinyengo, kutukwana, ziwawa, kumenyana ndi zikwanje ndi zina pomwe dziko likuwadziwa koma kumawasekelera kuti azipitiliza.

Pomwe amayankhula pa mwambo okondwelera kuti dziko lino latha zaka 61 lili pa ufulu odzilamulira, a Chakwera anatsindika kuti dziko lino likuyenera kukhazikika pa maziko anayi omwe ndi; Chikhalidwe, Chiyembekezo, Chilungamo ndi Mtendere pomwe ati kumanga molimba mazikowa nkofunika kufatsa.

Iwo anati dziko lopanda maziko anayiwa limavuta kutukuka kwake, limagwa mphwayi komanso limakhala la ziwawa.

“Maziko a chinayi ndi mtendere, tiyiwale kuti titukula dzikoli pomenyana ndi dzikwanje, kapena ziwawa pa zinthu zomwe sitinagwirizane nazo,” anatelo a Chakwera.

Mtsogoleriyu poyankhula pa mwambowu ku bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe anatinso poteteza mtendere mdziko muno, aMalawi adzitha kukambirana, kulekana ndi kuti chilichonse chikachitika athamangile ku mabwalo a milandu, kulemba pa masamba a mchezo, kukachita ziwonetselo ku nseu, kumangana ndi unyolo mwa zina.

M’mawu ake mtsogoleri wa dziko la Botswana Duma Gedion Boko wafunira dziko lino masankho a mtendere mu mwezi wa September.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading