
Mtsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera watchula zinthu zingapo zomwe wati zikusokoneza chitukuko cha dziko lino kupita patsogolo.
Poyankhula pa bwalo lazamasewero la Bingu mumzinda wa Lilongwe pomwe pali mwambo okumbukira ufulu odzilamulira tokha, Chakwera anatchula mtendere ngati chimodzi mwa zomwe zingatengere dziko lino patali.
“Ntchito yomanga maziko a dziko lino ikufunika mtendere. Akulu akale anati nkhondo simanga mudzi, ndiye tikapitiliza khalidwe loti tizimenyana ndizikwanje pazilizonse zomwe tikutsutsana dziko silingatukuke.
“Sikoyenera tikasemphana maganizo kumangothamangira kumabwalo a milandu, m’masamba a mchezo kukatukwana kapena kunsewu kukayambitsa ziwawa. Chofunika ndikukambilana mwa mtendere,” anatero Chakwera.
Mwazina, Chakwera watinso aMalawi akuyenera kusintha makhalidwe awo pofuna kumanganso maziko wolimba a dziko lino.
“Khalidwe lowononga zitukuko zomwe boma likuchita, khalidwe longofuna za ulere osafuna kugwira ntchito, nthawi zonse kufuna kutchelana misampha, izi sizingathandize kukonzaso maziko a dziko lino,” anonjezera a Chakwera.
Chakwera anapemphanso aMalawi kukhala ndichiyembekezo komanso chilungamo pofuna kukonzanso mazikowa.
Mtsogoleriyu wati zonsezi zikufunika kuzikonza modekha kamba koti kumanga maziko mwaphuma ndi ngozi yayikuru.