Kutola ma point mu TNM Super League kukuvuta chaka chino – Mpulula


Leo Mpulula is coach for Tigers which play in the Super League of Malawi

Mphunzitsi wa timu ya WakaWaka Mighty Tigers, Leo Mpulura wati ngakhale lero apeza ma point onse atatu pa Mzuzu City Hammers koma kupeza ma point mu TNM Super League yachaka chino kukuvuta.

Tigers yadya kudzera mu chigoli cha captain Kelvin Banda pa mphindi ziwiri zoyambilira pomwe Greyson Msowoya anagwetsedwa pa mbuto yolakwika masewelo omwe anali pa bwalo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre.

Mphunzitsi Mpulura wati anyamata ake akwanitsa kutenga ma point onse pa Mzuzu City Hammers ngakhale kutenga ma point mu ligi ya chaka chino kukukhala kovuta.

Mpulura wati timu yake sinali pabwino pa mndandanda wa ma timu onse 16 ndipo kupambana kwa lero kuwonjezera mphamvu kwa osewela.

Mphunzitsiyu watinso anyamata ake akuphonya kwambiri, mwakuti mipata yomwe anali nayo m’masewelowa amayenera kupambana ngakhale mu gawo loyamba lomwe, koma mphumi ndi mwayi ndi zomwe analibe chabe masewelo a lero.

Mphunzitsi wa Mzuzu City Hammers, Elias Chiyambo wati Tigers sinali yowopsa kwambiri ngakhale agonja pomwe wati wawona mavuto mu timuyi omwe akonze poti awa anali masewelo ake oyamba chibweleleni ngati mphunzitsi.

Iye wati timu ya Mzuzu City Hammers ndi yabwino. Hammers yomwe chiyambileni cha masewelo a mu ligi yangopambana masewelo awiri okha, tsopano yatsakamira pa nambala 15 ndi ma point ake asanu ndi atatu (8).

Kupambana kwa Wakawaka Mighty Tigers tsopano kwakankha timuyi kufika pa nambala 11 ndi ma point ake 13.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading