Mighty Wanderers ikukana kugonja, yatolako pa Karonga United

Advertisement
Wanderers

Timu ya Mighty Wanderers ikukanabe kugonja pomwe m’masewelo ake lero ndi Karonga United agawanako ma point 1-1 mu masewelo a mu 2025 ipemelele TNM Super League.

Zigoli zonse mchigawo choyamba kuchoka kwa Gadie Chirwa ndi mutu wake komanso Alfred Chizinga kudzera pa penate nzomwe zakanikitsa Wanderers kutola onse ma point pa bwalo la Karonga komanso kukana kugonja m’masewelo 9.

Mphunzitsi wa Karonga United, Oscar Kaunda wati masewelo a lero anali abwino ndipo ati achita bwino kutolako point pomwe akuchokera kogonja komanso pomwe amenya masewera atatu masiku asanu ndi awiri komanso ati ayenda maulendo atali atali.

Kaunda wati akuyang’ana kuti pomwe ligi idzitha gawo loyamba akhale ali ndi ma point oposa 20.

Mphunzitsi wa Wanderers, Bob Mpinganjira wati ngakhale anyamata ake anali ochepa koma anawonetsa mtima odzipeleka ngakhale mwayi sunawagwele kweni kweni.

“Kupeza point sichinthu cholakwika kweni kweni maka kupeza koyenda, chifukwa zakoyenda sunganeneletu,” anatero Bob Mpinganjira.

Osewera Timothy Silwimba ndiye amene wasankhidwa kuti wasewera mwapamwamba kuposa anzake onse.

Masewelo asanu ndi anayi (9) Mighty Wanderers sinagonjebe ndipo pano tsopano ili pa nambala yachiwiri ndi ma point ake 23 kulekana point imodzi ndi FCB Nyasa Big Bullets yomwe ili ndi ma point 24.

Karonga United ili pa nambala 5 ndi ma point ake 16

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.