
Yemwe akudzapikisana nawo pa mpando wa phungu wa nyumba ya malamulo ku dera la Machinjiri mu mzinda wa Blantyre, Veronica Ndalama, wati nkofunika kwambiri kuwapatsa achinyamata zochita zaphindu ngati njira imodzi yochepetsera makhalidwe oyipa.
Ndalama yemwe ndi wa chipani cha Democratic Progressive, wanena izi Lamulungu pa bwalo la Nthawira Parish ku Machinjiri Area 3 munzinda wa Blantyre, pamene amakhazikitsa chikho cha mpira wa miyendo komaso wa manja cha ndalama zokwana K20 miliyoni.
Iwo ati aganiza zokhazikitsa chikhochi chifukwa awona achinyamata ambiri akungokhala ndipo mpikisanowu uwapezetsa mwayi otakataka ndi kupewa kuchita zoipa.
“Ndakhazikitsa ligiyi pofuna kuthana ndi makhalidwe oipa komanso kupezetsa zochita anyamata omwe akungokhala mu dera muno” watelo Ndalama.
Ma timu 73 ampira wa miyendo komanso 18 a mpira wa manja akhala akulimbilana chikhochi kufikika mwezi wa August ndipo ma timu onsewa apatsidwa 50,000 kwacha komanso mpira umodzi ngati njira imodzi yowalimbikitsa kuti achite bwino pa masewero awo.