Mighty Wanderers yawaza Dedza Dynamos kuzula Bullets pa nambala 1

Advertisement
Wanderers

Mighty Wanderers tsopano ili pa tsogolo mu mndandanda wa ma timu a mu TNM Super League pomwe ili ndi ma point ake 22 ndi kukaniratu kugonja chiyambileni league.

Zigoli za Promise Kamwendo pa mphindi ya chi 7 ndi Isaac Kaliati pa 56 zapatitsa Wanderers ma point onse atatu ndi kuyichotsa FCB Nyasa Big Bullets yomwe imatsogolera mndandanda ndi ma point ake 21 onse m’masewelo 8.

Mphunzitsi wa Premier Bet Dedza, Dynamos Alex Ngwira wati zigoli zomwe agoletsetsa angopeleka ngati mphatso chifukwa mipata yonse yomwe anapeza akanika kuyisintha kukhala zigoli chifukwa zawonekeratu kuti anyamata ake anapeleka ulemu.

“Anyamatawa lero sanandisewelele m’mene ndimafunira koma tikonzamo muwonanso tikhala tikumenya bwino,” Ngwira watero.

Bob Mpinganjira mphunzitsi wa Mighty Wanderers wati masewelo ake ndi Dedza sanali ophweka koma anyamata analimbika mtima.

Mpinganjira wati anyamata ake akumachita bwino ndipo akumvera zomwe akuwuzidwa, iye wati ulendo udakalipo zomwe zikufunika kuti achilimikebe.

Mu masewelo a pa bwalo la Kamuzu, Isaac Kaliati ndi amene wasankhidwa kukhala osewera wapamwamba kuposa anzake.

Dedza ili pa nambala 7 ndi ma Point ake 13, ndipo Alex Ngwira tsopano wagonja koyamba chibweleleni Ku Dedza kudzatenga malo a Andrew Bunya yemwe anamuthamangitsa chifukwa cha kusachita bwino kwa Dedza Dynamos.

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.