MCP ikuwatenga a Malawi ngati opusa – Msaka

Advertisement
Msaka

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) mchigawo cha kum’mawa, Bright Msaka, wati chipani cha Malawi Congress (MCP) chikuwatenga a Malawi ngati opusa powalonjeza zinthu zomwe chipanichi sichinakwanilitse angakhale chinthu chimodzi chokha.

Poyankhula pa msonkhano omwe chipanichi chinachititsa Loweluka pa bwalo la sukulu ya pulaimale ya Zobwe, m’dera la Zomba-Changalume, Msaka anati mwachitsanzo, a MCP analonjeza feteleza otchipa mtengo koma padakalipano, feteleza akugulitsidwa pa mtengo okwera kwambiri, zomwe ati aMalawi ambiri sakukwanitsa kugula.

Ndipo m’mawu ake, yemwe akuimira pa mpando wa phungu wa nyumba ya malamulo ku dera la Zomba-Changalume, Feston Kaupa, anadandaula kuti anthu ambiri m’derali ali pa njala ya dzaoneni chifukwa sanakwanitse kugula feteleza.

“Anthu a dera lino ndi okonda ulimi koma akanika kulima chifukwa anakanika kugula feteleza ndipo chipanda mapira, anthu ambiri akanafa ndi njala,” anatero Kaupa.

A Kaupa anatsimikiziranso anthu omwe anafika pa msonkhano-wu kuti asade nkhawa ndipo alimbe mtima chifukwa “Aiguputo” onsewa sadzawaonanso pa chipani cha DPP komanso mtsogoleri wake, Arthur Peter Mutharika akalowanso m’boma pa 16 September chaka chino.

Tinalephera kuti timve mbali ya chipani cha MCP chifukwa m’neneri wa chipanichi, Jessie Kabwira, samayankha lamya yake ya m’manja.

Ena mwa akuluakulu a chipani cha DPP omwe anali nawo pa msonkhano-wu ndi monga gavanala wa chipanichi mchigawo cha kum’mawa, Daud Chikwanje, mkulu wa amai mchigawochi, Elluby Kandeu komanso mkulu wa achinyamata mchigawochi, Steven Bamusi.

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.