
Mphunzitsi wa FCB Nyasa Big Bullets wayankhulapo pa zomwe zakhala zikumveka m’masamba a m’chezo kuti katswiri watimuyi wapakati, Lameck Gamphani akufuna kuchoka.
Poyankhulapo pa msonkhano wa olemba nkhani mu mzinda wa Blantyre Lachinayi, Mponda wati nkhani yakatswiriyu imafalitsidwa ndi anthu ongofuna kutchuka m’masamba a mchezo.
Iye wati anali odabwa kumva kuti Gamphani akunyanyala zokonzekera za timuyi chonsecho katswiriyu anali ovulala.
“Chomwe ndikudziwa ndichoti Gamphani anali ovulala ndipo azachipatala anamuuza kuti asasewere kwa sabata imodzi”
“Atachila anayamba kuchita zokonzekera, ndie sindikudziwa kuti mphekesera izi zikuchoka kuti, koma ndikukhulupira kuti awa ndi anthu chabe ongofuna kutchuka mmasamba awo amchezo” anatero Mponda.
Koma Mponda anati timu yake singatchingile osewera aliyense yemwe akudziwona kupelewela ndipo akufuna kukasewera kwina pangongole.
Iye anapitiliza kunena kuti FCB Nyasa Big Bullets ndi timu yayikulu ndipo singakakamize osewera yemwe sakukondwa, kukhalabe ku timuyi.
Gamphani anagulidwa ku timu ya Premierbet Dedza Dynamos pamsika wapakati pa chaka cha mpira cha 2024, ndipo nthawi imeneyo mphunzitsi wa Bullets anali Kalisto Pasuwa.