Akubanja ayimitsaso kunyamula thupi la malemu Edgar Lungu ku South Africa


Lungu

Mpungwepungwe siukutha ku Zambia pomwe akubanja la mtsogoleri wakale wa dzikolo Edgar Lungu ayimitsa dongosolo lonyamula thupi lake kuchokera ku South Africa ponena kuti boma laphwanya mapangano akuluakulu okhudza dongosolo la malirowa.

Malingana ndi wailesi ya BBC, zokonzekerazo zidamalizidwa ndipo thupi la malemu Lungu limayenera kufika ku Zambia Lachitatu pandege. Koma akubanja ayimitsa ndondomekoyi, ponena kuti zikuvuta kwambiri kukhulupirira kuti boma likwanilitsa mgwirizano wawo.

Mneneri wabanja Makebi Zulu, wati ndi odabwa kuti boma lidatulutsa ndondomeko ya malirowo, osakambirana ndi banjali. Mwazina, ndondomekoyi imasonyeza kuti mtsogoleri wa dzikoli Hakainde Hichilema ndiyemwe akalandire thupi la Lungu zomwe akubanja sakufuna.

“Zomvetsa chisoni kwambiri, kuti mtembo wa Purezidenti Edgar Chagwa Lungu subwerera lero,” Makebi Zulu yemwe ndi mneneri wa banjali adauza BBC. “Ndichiyembekezo chathu kuti tsiku lina thupi lake lidzabweretsedwa kumudzi ndikuikidwa m’manda.”

Lungu, yemwe adali mtsogoleri wa dziko la Zambia kuyambira 2015 mpaka 2021, wamwalira pa 5 June, 2025 pa chipatala china m’dziko la South Africa komwe adapita kukalandira thandizo.

Akubanja akuloza chala boma kuti lidalephera kumuthandiza Lungu pomwe amadwala, choncho akhala akukana kuti boma la Zambia lisatenge gawo lili lonse kapena kupeleka thandizo pa malirowa.

Sabata yatha mbali ziwirizi zidakambirana ndikugwirizana kuti mwambo wa malirowa ayendetsera limodzi koma akubanja adapeleka malire ku boma. Pano akubanja asinthaso mawanga pomwe akuti akuona kuti boma silikufuna kukwanilitsa mgwirizano wawo.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading