Nzika ku Area 54 zipanga m’bindikilo pochedwa kupatsidwa chipukuta misonzi pa malo awo

Advertisement
Palani

Anthu opitilira 3000 m’dera la Area 50 ku Lilongwe, alembera kalata Lawford Palani, Bwanamkubwa wa Khonsolo ya Lilongwe kumudziwitsa za m’bindikilo sabata ya mawa ino pa nkhani ya ndalama za chipukuta misonzi pa malo omwe boma lidawasamutsa.

Anthuwa omwe akuchokera kwa gulupu Kamphinda, Khongo, Katola, Dothi ndi Chinkhotankhazi kudera la mfumu yaikulu Chitukula m’boma la Lilongwe, akudandaula kuti sadapatsidwebe ndalama za chipukuta misonzi pa malo omwe boma lidawachotsapo mchaka cha 2022.

Iwo ati apanga chiganizo cha m’bindikilowu kamba kokwiya kuti masiku 7 omwe anapereka kwa nduna ya za malo a Deus Gumba kuti akhale atawapatsa ndalamazi atha koma palibe chomwe chachitika.

“Tikukudziwitsani kuti takonza mbindikiro omwe uchitike ku ofesi ya Bwanamkubwa wa Lilongwe Lolemba pa 23 June 2025 mpaka kulira kwathu kutayankhidwa,” yatelo kalata ya nzikazi. “Timati tikukumbutseni bwana Palani kuti kalatayi siyopempha chilolezo koma kukudziwitsani za m’bindikirowu.”

Anthuwa akumbutsa akuluakulu a boma kuti iwo sanapite ku boma kukasatsa malo awo, koma kuti bomalo linakachita kuwapeza iwo ndi kuwaretsa zomwe iwo amachita pa malopo kuti azipeza ndalama zosamalira mabanja awo.

“Lero pano tiri pa umphawi wadzaoneni chifukwa cha mtima wosalabadira anthu, choncho ife tidzaleka m’bindikirowu pokhapokha mutatipatsa chipukuta misozi basi,” zadandaula nzikazi.

Nkhaniyi ikukukhudza malo okwana mahekitala 1,020 pakati pa Malawi Institute of Management (MIM) ndi mphambano ya bwalo la ndege la KIA, m’mphepete mwa msewu wa M1 ku Lilongwe omwe adasankhidwa kukhala gawo la Area 54.

Anthuwa akudandaula kuti pomwe iwo sadapatsidwe chipukuta misonzi pochotsedwa pa malowa, boma layamba kugulitsa mbali ina ya malowa kwa anthu ena kuti apangepo chitukuko.

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.