
Anthu ambiri okhala m’boma la Zomba ati akuda nkhawa pa za chitetezo chawo pomwe mchitidwe ophana ukuwoneka kuti ukuchulukira tsopano.
Nkhawazi zadza pomwe lero anthu a m’mudzi mwa Njonjo ku dera la Chinamwali anadzuka ndi mantha atapeza mzimayi wina ataphedwa pochita kudulidwa pakhosi.
Nkhawazi zikudzanso kamba koti masiku ochepa apitawo anthu ena achifwamba awombera ndi kupheratu m’nyamata wina ochita ntchito za kabanza wa Njinga yamoto ku dera lomweli la Chinamwali.
Mneneli wa apolisi m’boma la Zomba a Patricia Sipiliano atsimikiza za kuphedwa kwa anthuwa.
Anthu ena apempha apolisi kuti akhwimitse chitetezo m’bomali pomwe ati mantha achuluka tsopano.