
Kulingalira za m’Malawi yemwe nkhondo sayidziwa ndipo akamva phoo! M’malo mothawa amathamangira komko! Kodi nanga ku Israel ndi ku Iran-ko a Malawi akupuma bwanji?
Pomwe nkhondo pakati pa mayiko a Israel ndi Iran yafika m’tsiku lachisanu, mayiko angapo ayamba kuthawitsa nzika zake kuchoka m’mayiko awiriwa.
Mayiko ngati UK, China, Poland, kungotchulapo ochepa chabe, analengeza kuti atumiza ndege kuti zikatenge nzika zake m’dziko la Israel ndicholimga chofuna kutateza kuti nzikazi zisakhudzidwe ndi nkhondoyi.
Naye mtsogoleri wa dziko la USA Donald Trump anachenjeza mzika zake kuti zisamuke mdziko la Iran makamaka mdera la Tehran. Nalo dziko la Thailand lati likukoza zokatenga nzika zake zonse m’mayiko a Israel komaso Iran.
“Ndife okozeka kukatenga nzika zathu ndipo tauza asilikali athu kuti pakhale ndege zomwe zikawatenge kuchoka ku Israel komaso Iran,” watelo Jirayu Houngsub mneneri wa boma ku Thailand.
Pakadali pano dziko la Malawi silinaotse chidwi chofuna kusamutsa nzika zake zomwe zili m’mayiko awiriwa. M’neneri mu unduna owoona za ubale wa dziko lino ndi maiko ena Charles Nkhalamba wati aMalawi omwe ali m’dziko la Israel ndi otetezeka.
Poyankhula ndinyumba zina zofalitsa nkhani mdziko muno, Nkhalamba wati ofesi ya kazembe wa dziko lino ku dziko la Israel akulumikizana bwino ndi aMalawi omwe ali m’dzikolo.
Malingana ndi wayilesi ya Aljazeera anthu opitilira 220 ndi omwe amwalira pofika pano m’dziko la Iran pomwe anthu oposa khumi ndi anayi ndi omwe amwalira m’dzikola Israel.