Makhonsolo bwezani K1.3 billion yathu yomwe mukulephera kuyifotokozera – yatero World Bank

Advertisement
Dedza District Council

Banki yayikulu pa dziko lonse – World Bank yalamula ma khonsolo mdziko muno kuti abweze ndalama zokwana 1.3 billion Kwacha za mndondomeko yothandizira kutukula miyoyo ya anthu pansi pa Social Support for Resilient Livelihood Project (SSRLP), kutsatira kawuniwuni yemwe wawonetsa kuti ndalamazo sizinagwiritsidwe bwino ntchito.

Izi zadza pomwe akatswiri a ku Bank yayikuluyi limodzi ndi Nation Local Government Finance Committee (NLGFC) ndi ma khonsolo anawunika m’mene ndalama zake zagwilira ntchito m’chaka cha 2021 kufika 2023.

Malinga ndi zomwe nyumba zina zotsindikiza nkhani mdziko muno, khonsolo ya Nsanje ikuyenera kubweza ndalama zokwana 169.1 million Kwacha yomwe 166 million Kwacha mwa ndalamayi khonsoloyi yakanika kupeleka ma umboni a momwe inagwilira ntchito.

Nayo khonsolo ya Dedza ati ibweze 93.1 million Kwacha chifukwa chosatsata ndondomeko ya momwe amagwiritsira ntchito komanso chifukwa chogwilitsa ntchito zikalata zina zolipilira ogwira ntchito zosavomelezeka.

Bank-yi yati kuwunika za ndalamazi kunali kofuna kupeza zoona za kagwilidwe ntchito ka ndalama zake ndipo papezeka zolakwika zochuluka zofuna mayankho, komanso ati apeza kuti ma khonsolowa akanika kutsata ndondomeko zomwe anagwirizana ndi zomwe zili mu kalozera wa kagwiritsidwe ntchito.

Malinga ndi World Bank, ma khonsolo onse omwe akhudzidwa ndi nkhaniyi apatsidwa malire pa 30 June kuti akhale atabweza ndalamazi.

Bank- yi yatinso ma khonsolo akhazikitse kafukufuku wa pa khonsolo ndi kawuniwuni wa chuma pofuna kupeza momwe ndalamazi zimatulukira mopanda dongosolo, ndipo ogwidwawo akuyenera kulandira zilango zowayenera.

Ngati njira imodzi yofuna kuthana ndi mchitidwewu, ma khonsolo ati tsopano akuyenera adzipeleka ndondomeko ya chuma yowunikidwa bwino pomafika pa 10 mwezi uliwonse.

Advertisement

One Comment

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.