Kwatuluka zikwanje ku Mzuzu

Advertisement
panga knife

Pomwe gulu lina la anthu limayenda m’misewu kufuna kulepheretsa ziwonetsero zomwe anakoza anthu ochita malonda munzinda wa Mzuzu, nawo ochita malondawa akatulutsa zawo zikwanje.

Mavenda akufuna kuchita zionetserozi posakondwa ndi kukhala chete kwa boma pa madandaulo omwe iwo akuti adapeleka miyezi yapitayi pa nkhani ya kukwera mtengo kwa katundu osiyanasiyana.

Anthuwa ati akufuna nduna ya zamalonda ndi mafakitale a Vitumbiko Mumba, nduna ya zachitetezo m’dziko Ezekiel Ching’oma, komanso nduna ya za maboma a ang’ono a Richard Chimwendo Banda kuti atule pansi maudindo awo ponena kuti sakuwathandiza pa madandaulo awo.

Koma zionetserozi zisanayambike gulu lina la anthu onyamula zikwanje linalowa mumzinda wa Mzuzu kufuna kulepheretsa ziwonetsero zomwe mavendawo akonza. Izi zimachitika ngakhale apolisi anali balalabalala munzindawu.

Posakhalitsa nawo mavenda motsogozedwa ndi atsogoleri awo Alexander Sikwese ndi a Gerlad Maulana, anasonkhana ndikunyamula zikwanje zawo ndikumayenda molunjika komwe kunali gulu lina la zikwanjelo.

Malingana ndi Sikwese, iwo anyamula zikwanjezi ngati mbali yodziteteza okha pomwe akuti akhala akupitilirabe ndi zionetserozi.

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.