Kapena kukubwera Traore? Msilikali opuma apikisana nawo pa upulezidenti

Advertisement
Mvula

Pomwe masiku akupitilira kuthera ku chitseko kuti dziko lino lichititse chisankho, nambala ya anthu omwe apikisane pa udindo wa mtsogoleri wa dziko ikukwerabe pomwe Phunziro Mvula yemwe anakhalapo msilikali wa Malawi Defense Force (MDF) walengeza kuti apikisana nawo.

Poyankhula ndi nyumba zina zofalitsa nkhani m’dziko muno, Mvula wati mavuto omwe akuta dziko la Malawi pano akufunika munthu wapadera osati anthu omwe akhazikika mu ndale ponena kuti onse awonetsa kale kuti alephera kuphura dziko lino pa moto.

Kuwonjezera apo, kumayambiliro a sabata ino Mvula adalemba pa tsamba lake la fesibuku kuti ngati aMalawi akufuna kuti zinthu zisinthe, sakuyeneraso kuika zipani za Malawi Congress (MCP) komanso Democratic Progressive (DPP) m’boma.

“Ndiye tiyenera kuchita chiyani? Njira yokhayo yothetsera mavutowa ndikuchotsa m’boma lopanda nzeruli ndikuika boma latsopano. Ndikubwereza boma latsopano ndi anthu atsopano, pulezidenti wodziimira pa yekha wodziwa zambiri komanso wachifundo.

“Kumbukirani kusankha pakati pa MCP ndi DPP ndi chimodzimodzi kusankha kolera m’malo mwa tayifodi (typhoid) zomwe zonse zitha kukuphabe. UTM siyoyeneranso chifukwa ndi mbali ya chiwiri ya DPP,” watelo Mvula muuthenga omwe analemba m’chizunga pa tsamba lake la fesibuku.

Chiwerengero cha anthu onse omwe apikisane pa udindo wa mtsogoleri wa dziko pa chisankho cha pa 16 September pano, chidziwika mwezi wamawa pomwe bungwe la MEC likhale likulandira zikalata za onse omwe akudzapikisana.

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.