Sandram alonjeza kupitiliza kuthandiza chipatala cha South Lunzu

Advertisement
Sandram

Pali chiyembekezo kuti ntchito pa chipatala cha South Lunzu munzinda wa Blantyre zidziyendako bwino potsatira thandizo la ndalama zokwana K25 miliyoni lomwe Deus Sandram mogwilizana ndi OG Group of Companies komanso Build Africa apereka.

Sandram yemwe amatchuka ndi dzina loti “Obwande” ndipo akudzapikisana pa mpando wa phungu wa nyumba ya malamulo m’dera la South Lunzu pachisankho chikubwerachi, wati wapanga izi kamba ka chidwi chake chofuna kuthandiza anthu m’derali.

“Ndabweletsa chitukukochi m’dela lino pofuna kuthandiza mavuto omwe chipatalachi chimakumana nawo, ndipo tikhala tikukonza misewu komanso polisi mu dela lino,” watelo Sandram.

Mkulu wa malonda ku OG Group of Companies, Tikambe Kachali wati sikoyamba kugwila ntchito zachifundo ndipo wati ali ndi masomphenya othandiza chipatalachi ndi katundu komanso zitukuko zosiyanasiyana.

“Takonza chipatalachi mothandizana ndi kampani ya Build Africa ndi ndalama zokwana K25 million ndipo tili ndi masomphenya opitiliza kuthandiza chipatalachi pomanga mpanda, kupeleka mipando ya plastic komanso ma desk atsopano,” walonjeza Kachali.

Oscar Soko yemwe amayang’anila chipatala cha South Lunzu wati ndiokondwa kwambiri kamba ka thandizoli ndipo wapempha enaso akufuna kwabwino kuti atengere chitsanzo zomwe wapanga Sandram ndi makampaniwa.

“Tikusowekera thandizo la galimoto yonyamula odwala, matilesi ogonela mu chipinda cha amayi oyembekezela komanso mankhwala mu chipatalachi,” anapempha a Soko.

Mwazina, ndalamayi yagwira ntchito yopentaso chipatalachi, kuikira zitseko komaso bolodi (white board) zatsopano, komaso kuika thanki losungira madzi la malita 5000 kuti madzi asamasowe pa chipatalachi.

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.