Wandale amene sanaulule chuma chake asavoteledwenso, adye zomwe wabazo – George Phiri

Advertisement
Phiri

Katswiri pa ndale ndi ulamuliro wabwino a George Phiri ati pamene dziko likupita ku masankho a pa 16 September, aMalawi sakuyeneranso kusankha andale onse omwe anakanika kuwulura za kuchuluka kwa chuma chawo pomwe anasankhidwa mbuyomu, ponena kuti anabisa ncholinga choti awabele aMalawi.

A Phiri ati andalewa anawona kuti nkwabwino kuti abise za chuma chawo kuti aMalawi akanike kufunsapo, pomwe ati andale ambiri amakonda za m’dima, kuba komanso ziphuphu.

Polankhula mu pologalamu ya pressing issues pà wayilesi ya Kasupe, katswiriyu wati andalewa ngakhale ayesetse kubweza zomwe anabazo popeza ndi nyengo yokopa anthu, aMalawi akumbukire kuti wakuba ndi wakuba ndipo wakuba ndi oyipa,

A Phiri ati ndale asamaiwale kuti mphamvu zawo zomwe amapatsidwa zimakhala zobweleka kwa anthu ndipo nthawi ikadakwana kuti andalewa adzimva kuwawa monga mmene amamvera owasankha.

M’mawu awo a Phiri anati andale amakanika ngakhale kuyika zinthu poyera kawirikawiri popeleka zitsanzo za kagwiritsidwe ntchito ka ndalama za maulendo ndi zina.

“Ngati anthu ambiri akumva kuwawa ndekuti wandale amene ali pa udindo nthawi imeneyo ndi oyipa, kotelo kuti anthu oyipa safunika pa udindo, andale sawulura za ndalama zomwe akugwiritsa ntchito mu maulendo,” anatelo a Phiri.

Mabungwe ambiri mdziko muno monga la Malawi First motsogozedwa ndi a Bon Kalindo, bungwe la CDEDI motsogozedwa ndi a Sylvester Namiwa akhala akupempha nthambi ya boma yomwe imayang’anira zowunika katundu wa ogwira ntchito m’boma kuti ichilimike pokakamiza andale kuti awulule za chuma chawo.

Nthambi ya Office of the Director of Public Officer’s Declaration (ODPOD ndi yomwe inapatsidwa mphamvu ndi malamulo a dziko kuwunika katundu yemwe anthu ogwira ntchito m’boma alinaye komanso kutsimikizira ndi kupeleka m’manja mwa oyenera kwa amene akukanika kufotokoza za chuma chawo kuti malamulo agwira ntchito pa iwo.

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.