Akakuputani musawabwenzele chipongwe – Chisale

Advertisement
Chisale

Mkulu wa achinyamata mchipani cha Democratic Progressive (DPP), Norman Paulos Chisale, walangiza achinyamata komanso anthu onse otsatira chipanichi kuti asamabwenzere mchitidwe wa chipongwe komanso zipolowe zomwe otsatira zipani zina akuwachitira pamene dziko lino likukonzekera chisankho cha pa 16 September, 2025.

“Tiyeni tipitilize kukhala anthu a mtendere.Sitiyenera kulimbana nawo kapena kubwezera mchitidwe wa chiwawa.Tikumbukire kuti DPP imayimira mtendere ndi chitukuko.

“Akakuputani muzingowayang’ana ndipo chonde, osawabwenzera chipongwe,” anafotokoza Chisale.

Iwo anayankhula izi Loweruka masana pa msonkhano omwe achinyamata a chipanichi anakonza m’boma la Balaka. A Chisale anatsindika kuti akudziwa bwino lomwe kuti zipani zina zandale zakangalika kuyambitsa zipolowe pofuna kusokoneza bata ndi mtendere.

Izitu zikudza pamene mchitidwe wa zipolowe zokhudza ndale wamanga nthenje m’dziko muno ndipo nthawi zambiri, oyambitsa ake amakhala achinyamata.

Pa msonkhano-wu, Hopeson Nazombe, yemwe ndi wapampando wa achinyamata a chipanichi ku Balaka wati achinyamata-wa amalemekeza malamulo ndipo ndi okonzeka kuwonetsetsa kuti sakukhudzidwa nawo mu mchitidwe ulionse wa ziwawa.

“Ife timayendera malamulo, chomwe tikufuna ndi chakuti DPP ibwelere m’boma kudzera mu njira yachilungamo, osati chiwawa,” anafotokoza Nazombe.

Pambuyo pa msonkhano-wu, achinyamata-wa anapereka thandizo la chakudya komanso katundu osiyanasiyana kwa odwala pa chipatalapa chachikulu cha boma cha Balaka.

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.