Namalomba adzudzulidwa poyankhula udyo

Advertisement
Namalomba

Mneneri wachipani chotsutsa boma cha Democratic Progressive (DPP), Shadreck Namalomba, akudzudzulidwa kamba kazomwe walankhula pa nkhani ya imfa za anthu angapo omwe anali otsatira chipani cha Malawi Congress (MCP).

Potsatira imfa ya wachiwiri kwa nduna yowona zamaboma ang’ono Joyce Chitsulo, Lachisanu a Namalomba adalemba pa tsamba lawo la Facebook kudandaula kuti anthu andale angapo adamwalira mosavetsetseka atangolowa chipani cha MCP.

“Sidik Mia yemwe adali membala wachipani cha DPP adalowa chipani cha MCP ndipo adakwera nkufika paudindo wa Vice President. Komabe, moyo wake unafupikitsidwa modabwitsa.

Saulos Chilima, yemwe anali wodziwika bwino mu DPP ngati wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko, adapanga mgwirizano ndi MCP kudzera mu chipani chawo cha UTM. Tsoka ilo, anakumana ndi imfa yake yosayembekezereka pa ngozi yomvetsa chisoni ya ndege,” walemba choncho Namalomba.

Iwo ati imfa za anthu amenewa ndizovetsa chisoni komanso zopatsa mafuso ambiri. “Imfa zomvetsa chisonizi zikudzetsa mafunso oti nchifukwa chiyani chipani cha MCP chokha chili pachimake pamavuto otere.”

Koma anthu ochuluka omwe ayikira ndemanga pa tsambali, adzudzula Namalomba ponena kuti uku sikuyankhula kwa bwino.

“A Namalomba usawoneke wochenjera lero pomwe aliyense akudziwa bwino lomwe kuti mu nthawi ya ulamuliro wa DPP anthu ankafadi imfa zodabwitsa kwambiri ali m’manja mwa apolosi kapena kuchita kukonzedwa,” watero Andrew Masina. “Ife sitinaiwaletu imfa ya Issa Njaunju, Buleya Lule, Maxson Mbendera, Robert Chasowa omwe adachita kuphedwa.”

Naye wachiwiri kwa mneneri wa chipani cha MCP Ken Nsonda wati malankhulidwe a Namalomba akungowonetseratu kusakhwima nzeru pa ndale ponena kuti imfa ndi chinthu chomwe aliyense amasowa nacho mayankho poganiziranso pa zomwe zidakhala zikuchitika mma ulamuliro apitawa.

“Malemu Bingu wa Mutharika adachoka mchipani cha UDF ndikuyambitsa chawo cha DPP ndipo kenaka adamwalira ali mtsogoleri wa dziko lino. Kodi tidziti a Bingu adamwalira mosadziwika kapena achimwene awo a Professor Peter Mutharika ankadziwapo kanthu pofuna kuti akhale mtsogoleri wachipanichi?” watelo Nsonda.

Nsonda adati sakufuna kuyankhulapo zambiri pa nkhaniyi ponena kuti kutelo kukhala ngati kulemekeza malankhulidwe a munthu yemwe adakali wachisodzera pa ndale.

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.