Namiwa adzudzula Usi pomayenda ndilikukumwe la asilikali pa zinthu za zii

Advertisement

Mtsogoleri wa bungwe la CDEDI, Sylvester Namiwa wati zomwe akuchita wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Michael Usi, kumayenda ndi chinantindi cha asilikali pa zinthu za zii, ndizokhumudwitsa komanso zovetsa chisoni.

Izi zikudza pambuyo pa kanema wina yemwe anthu akugawana m’masamba anchezo, yemwe akuonetsa Usi akuyenda mozungulilidwa ndi khwimbi la asilikali pomwe amachoka ku msika kokagula nkhuku.

Namiwa
Namiwa: Kokagula matemba mpaka asilikali 100?

Poyankhula pa nsonkhano wa atolankhani Lachisanu ku Lilongwe, Namiwa wati izi nzovetsa chisoni kwambiri ponena kuti dziko la Malawi ndi la bata ndi mtendere choncho Usi samayenera kumatenga asilikali ochuluka chonchi.

“Zoona dziko la bata ndi mtendere ngati lino wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko azikayenda ndi asilikali oposa 100 kukagula mpiru, kukagula nkhuku, kumakadukula mu nsewu, tili siliyasi koma ngati dziko?” wadabwa Namiwa.

Iye wadandaulira mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera komaso ma bungwe kuti achitepo kanthu ponena kuti zomwe zikuchitikazi ndikuononga ndalama za misonkho ya aMalawi.

“Akumayenda ndi asilikali opitilira 100, nde mudziwe kuti msilikali aliyese amalandira alawasi,” watelo Namiwa. “Ndifuse kwa Chakwera, ku Judiciary, ku Parliament, ku Malawi Law Society kuti zoona tikuonelera Usi kumatenga asilikali kumakagula matemba? Umu ndi m’mene akuyenera kugwilira ntchito yake? Tonse lero a Malawi tichite manyazi.”

Namiwa wati mavuto osiyanasiyana akupitilirabe kukuta dziko lino kamba koti m’dziko muno mwachuluka, “kupusa, mantha komaso dyera.”

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.