
Boma lati liri ndichidwi komaso likufuna kuti dziko lino likhale patsogolo pa ntchito za luso lamakono, pofuna kukwanitsa masomphenya a chitukuko a 2063.
Mmodzi mwa akuluakulu oyang’anila za luso lamakono ku bungwe laboma la Electricity Supply Cooperation of Malawi (ESCOM), Nkwachi Theu, ndiyemwe wayankhula izi pa mkumano omwe bungwe loyang’anira zamaluso amakono la ICTAM, likuchititsa mumzinda wa Lilongwe.
Theu wati mwazina, zomwe boma likuchita pofuna kutukula ntchito zamaluso amakonowa, ESCOM yatsekulira ntchito yolumikiza intaneti yotchipa komaso yosadukaduka kwa a Malawi.
“Tabweretsa intaneti yolumikiza nthambo mmanyumba osati yomwe imalumikizidwa pa polo yopanda nthambo ija”
“Intaneti tikulumikizayi ndiyotsika mtengo komaso yosadukaduka olo kutakhala mphepo ngakhale mvula” anatero Theu.
Malingana ndi Theu, ntchitoyi inayamba pa 1 May ndipo anthu ena ku Blantyre komaso ku Mzuzu ayamba kale kuyigwiritsa ntchito.
Kupatula zomwe ESCOM ikupanga, Theu wayamikaso nthambi zina za boma ngati unduna wazamaphunziro komaso MACRA pobweretsa maphunziro a luso lamakono ku sukulu za pulayimale, ponena kuti izi zithandizira khumbo laboma kukwanitsidwa.
Ku msonkhano wa ICTAM omwe unayamba dzulo lachinayi ndipo ukuyembekezeka kutha lero, ESCOM yathandiza ndi K10 million komanso intaneti yaulere.