Kodi ndi bwino kusavota pa zisankho za pa 16 September chaka chino?

Advertisement
Elections

Ndakhala ndikumva maganizo a aMalawi ambiri kuti akhala akuvota kambirimbiri koma palibe m’moyo mwawo chasintha.

Ena akhala akudandaula kuti kuvota kumangothandiza atsogoleri kuti akhale paudindo ndi kumangodyerera kuiwala amene anawavoterawo.

Chifukwa cha izi, ena akuganiza kuti ndi bwino kuti chaka chino asavote.

Choyambirira, dziwani kuti ndi udindo wa mzika iliyonse imene idzakhale itakwanitsa zaka 18 pa 16 September kukavota.

Ngakhale palibe lamulo lokakamiza mzika kuvota, kusavota kumabweretsa mikwingwirima yosiyanasiyana.

Choyamba, ngati mzika  sikuvota, ndiye kuti akuchepetsa mwayi wowina wa atsogoleri awo. Izi zimapangitsa kuti zofuna zawo za amzika ziponderezedwe.

Chachiwiri, pamene munthu sanavote sakhala ndi chidwi choonetsetsa kuti atsogoleri akulamula bwanji. Izi zimapangitsa kuti ulamuliro woipa, wakuba, waukatangale ndi waumbava kuti uzipitilira.

Pamene anthu ambiri sanavote, wowinayo nthawi zambiri sakhala kuti wakondedwa ndi anthu ambiri mu dziko.

Kuphatikiza apo, kusavota kumaphwanya ufulu wa demokalase umene mzika ili nawo. Izi zimathandizanso kuti atsogoleri ndi mabungwe kuti akhalenso osasamala pa mfundo za demokalase.

Pamene anthu ambiri asakutenga mbali mu zisankho, anthu ndi magulu amatengerapo mwayi kuti akwaniritse zolinga zawo ngakhale zili zosakomera anthu ambiri.

Kuonjezerapo apo, mzika zimene sizitenga mbali pa zisankho zimataya mwayi  woika maganizo awo poyendetsera dzilo kapenanso kusintha tsogolo la dziko lawo.

Nthawi zinanso kusavota kumatanthauza kuti anthu sanawazindikiritse bwino za udindo wawo wovota.

Potsira mkota, sibwino kuti mzika isakavote. Tiyeni tikavote pa 16 September kuti tikasankhe mtsogoleri wa dziko, phungu wa nyumba ya malamulo ndi khansala wa ku mtima kwathu.

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.