A m’ndende 23 asemphana ndi mayeso a boma a JCE chaka chino

Advertisement
Zomba prison

A m’ndende okwana makumi awiri ndi atatu (23) asemphana ndi mayeso a boma a Junior Certificate of Education (JCE) a chaka chino cha 2025 mndende zisanu ndi imodzi za mdziko lino.

Mneneli wa nthambi ya Mndende, a Steve Meke ati Ndende za mdziko lino zinalembetsa ophunzira a mndende okwana 75 kuti alemba mayenso a JCE koma 52 okha ndi omwe alembe mayeso kutsatira kutha kwa zilango za a mndende 23 enawo.

Poyankhula pomwe mayesowa ayamba lero, a Meke ati ophunzira a mndendewa alemba mayenso mu Ndende za Zomba, Maula, Mzimba, Bvumbwe, Mzuzu, Chichiri ndi Ndende yosunga amayi ya Kachele.

Mneneliyu watinso omwe akulemba mayeso abomawa atenge mayesowa kukhala chinthu cha mwayi pomwe apatsidwa mpata owonetsa kuthekera kwawo pa maphunziro.

Iwo atinso kukonza umoyo wa okhala mndende kumathandiza kwambiri umoyo wa iwo maka akatuluka mndendezi, ponena kuti amakhala akutuluka koma ali ndi tsogolo pa maphunziro ndi maluso a zinthu zowapatsa ndalama zomwe zimachepetsanso kupalamula.

Nthambiyi yamika onse amene amatenga gawo pothandizira a mndende pa maphunziro.

Malinga ndi bungwe loyendetsa mayeso mdziko muno la Malawi National Examination Board MANEB, Ophunzira okwana 166,123, ndipo 85,902 mwa iwo ndi akazi, 80, 221 ndi amuna, chiwelengelo chomwe mchokwera kulekana ndi chaka chatha pomwe olemba mayesowa anali 163,950 onse.

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.