
Bungwe loyendetsa zisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) lati wapampando wa bungweli a Annabel Mtalimanja sanatule pansi udindo ngati wapampando.
Malingana ndi mneneli wa bungweli, Sangwani Mwafulirwa, wati anthu ena akufalitsa uthenga wa bodza kuti a Mtalimanja atula pansi udindo. Iwo ati wapampandoyu akugwirabe ntchito zake monga wa pampando malingana ndi malamulo.
A Mwafulirwa atsindika kuti mu nyengo ino yomwe dziko likuyandikira kupita ku masankho, kupeka kapena kusinjilira uthenga wabodza kumasokoneza anthu komanso ndondomeko ya chisankho.
Izi zikudza pomwe pamasamba a mchezo payenda nkhani yoti wapampando wa bungweli a Annabel Mtalimanja wapita kukatula kalata kwa mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera yotula pansi udindo.
Magulu ambiri ndi mabungwe ena mdziko muno akhala akulankhulapo ndi kufuna kuti wapampando wa MEC atule pansi udindo wake.