Joseph Kamwendo wavomeleza kuti Creck Sporting sinachite bwino

Advertisement
Kamwendo

Yemwe anali mphunzitsi wa timu ya mu mzinda wa Lilongwe ya Creck Sporting Club, Joseph Kamwendo wati chigamulo chakuchotsedwa ntchito kwake n’chosadabwitsa chifukwa chiyambileni ligi chaka chino timuyi yakhala isakuchita bwino.

Mphunzitsiyu yemwe anachotsedwa ntchito limodzi ndi omuthandizira ake awiri Abel Mkandawire ndi Chiukepo Msowoya wati Creck sinayambe bwino chiyambileni season ya mpira ya 2025.

Kamwendo wayamika utsogoleri wa timu ya Creck pomukhulupilira kuti atumikire ngati mphunzitsi wa timuyi pomwe wati wavomeleza zotsatira zomwe zadza ku mkumano wa akulu akulu pambuyo pa kuyimitsidwa ntchito.

Mlembi wa Cleck, Àaron Kandiwo Mtaya, wati timuyi tsopano ikusaka mphunzitsi amene angatenge timu ya Creck Sporting kupita kutsogolo m’malo mwa a Kamwendo, ndipo ayamikira kukhala bwino komwe kunalipo ndi mphunzitsi wakaleyu pomwe afunira zabwino aphunzitsiwa ochotsedwawa.

Kamwendo anamuyimitsa pa ntchito sabata lapitali chifukwa cha kusachita bwino kwa timu ya Creck pomwe idatuluka mu Airtel Top 8 itaswedwa ndi FCB Nyasa Big Bullets komanso kungopambana masewelo amodzi okha mu ligi m’masewelo anayi.

Loweluka lino timu ya asilikali ya MAFCO yayitana timu ya Creck Sporting kuti alimbilane ma point atatu mu TNM Super League pa bwalo la chitowe.

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.