
Phungu wa Nyumba ya Malamulo m’dera la kumadzulo kwa mzinda wa Lilongwe, George Zulu, wadzudzula zipolowe zokhudza ndale ku dera la Mtandire-Mtsiriza lomwe ayimire chaka chino.
Zulu wayankhula izi kutsatila zomwe zinachitika dzulo Lachiwiri, pomwe anthu omwe akuganiziridwa kuti ndiomutsatira ndi otsatira Ruth Chingwalu yemwe akuyimira nawo, amasinthana zibakera pa mwambo wa maliro ku Mtandire.
Zulu wati posatengera kuti anthuwo ndi wotsatira ndani, iye siwokondwa ndi zomwe zinachitikazi.
“Pomwe izi zimachitika ndinali nditachokako ku maliroko ndiye sindingadziwe kuti amapanga zipolowe ndi ndani. Koma ine ngati mtsogoleri, ndine okhumudwa kuva nkhani zimenezi ku dela langa,” watero Zulu.
Zulu anapitiliza kupempha achinyamata kudelari kupewa kugwiritsidwa molakwika ndi anthu a ndale popanga ziwawa.
Phunguyu wapemphaso mafumu ku delari kuti azigwira ntchito yawo mosasankha mbali, pofuna kupewa kugawanitsa anthu.
Ndipo m’mau ake, wachiwiri kwa mtsogoleri wa Democratic Progressive Party (DPP) m’chigawo chapakati, Alfred Gangata, wayamikira otsatira chipani chake, kamba koti sakumakhudzidwa pa nkhani zotere.
Gangata, yemwenso akuyimira pa mpando wa phungu ku delari, wapempha omutsatira onse kupitiliza kusunga bata ndi mtendere, akayambapo ntchito yokopa anthu kudelari.