
Adindo apemphedwa kuchitapo kanthu pa chitetezo ku manda a Henry Henderson Institute (HHI) munzinda wa Blantyre, pomwe malipoti akusonyeza kuti akathyali akupitilirabe kuwononga ndikuba zipangizo pa ziliza.
Mayi wina yemwe ndi m’modzi mwa anthu omwe ziliza za abale awo zakhudzidwa ndi umbandawu, wati anthu awupanduwa awononga chiliza cha malemu amunake chomwe chakonzedwa mwezi wa December, chaka chatha chomwechi.
Kudzera pa tsamba la fesibuku la Onjezani Kenani, mayiyu wati anthu omwe achita chipongwechi, aba zitsulo zomwe zinagwiritsidwa ntchito pokoza chilizachi. Iye wapempha khonsolo ya mnzinda wa Blantyre kuti ichitepo kanthu pa nkhaniyi.
“Khonsolo ya mzinda wa Blantyre, ndikukupemphani mwaulemu kuti muchitepo kanthu pofuna kulemekeza abale athu omwe anatisiya. Nchifukwa ninji anthu a moyo akusokoneza mtendere wa anthu akufa?” wafusa mayi wokhudzidwayu.
Naye Mada Chinguwo walemba pa tsamba lake la fesibuku kuti chiliza cha malemu bambo ake chakhudzidwa ndi mchitidwewu. Iye wati chodandaulitsa nchoti akuluakulu ena akudziwa za vutoli koma sakufuna kuchitapo kanthu.
“Amalume anga (omwe anapita kukaona ziliza za mayi anga ndi bambo anga) atafusa m’modzi mwa anthu osamalira ku mandawa, awuzidwa kuti khonsolo ya mzindawu ikudziwa za izi koma siikutumiza a chitetezo kuti adzikalondera,” wadandaula Chinguwo.
Poyankhula ndi tsamba lino, wofalitsa nkhani ku polisi ya Ndirande, Maxwell Jailosi wati pakadali pano sanalandire dandaulo lili lonse pa nkhaniyi.
Nkhani za kuonongedwa kwa ziliza ku manda a HHI, zakhala zikuvekaso m’mbuyomu. Kupatula manda a HHI, miyezi ingapo yapitayi, anthu ena omwe sadadziwikebe mpaka pani adaswanso ziliza zina ku manda a BCA munzinda omwewu.