MCP yagwiritsa ntchito dzina la Bakili Muluzi kuti anthu asakhulupilire DPP ku m’mawa


MCP

Mlembi wamkulu wa chipani cha Malawi Congress (MCP) Richard Chimwendo Banda wati anthu a m’boma la Mangochi sadzakhululukiranso chipani cha Democratic Progressive (DPP) chomwe chinamanga a Bakili Muluzi kwa zaka 17.

Poyankhula Lolemba pomwe amalandira mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera pomwe amafika m’bomali, a Banda ati chipani cha DPP chitamanga mtsogoleri wakale Bakili Muluzi, zinatengera ulamuliro wa a Chakwera kuyika a Muluzi pa ufulu.

Iwo ati a Chakwera anabwera kudzamasula unyolo omwe a Democratic Progressive (DPP) anamumanga nawo Bakili.

Apo ndi pomwe mlembiyu yemwenso ndi nduna ya maboma ang’ono anati ulamuliro wa a Chakwera wakonzeka kuchitabe zitukuko m’bomali kuphatikiza nseu wa Mangochi-Makanjira omwe ati ndalama zake zonse zinapezeka kale.

M’mawu ake mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera analimbikitsa kukhalirana mwa mtendere pakati pa aMalawi polewa kulankhulana mawu a chipongwe kwa ena.

Sponsored

“Amene tili ndi ma udindo, osalankhula ena udyo, udindo si chonyozera koma kutumikirana, kulolerana ndi kulemekezana potukula Malawi,” anatelo a Chakwera.

“Osachitilana nkhanza wina ndi mzake, osachitira nkhanza wina aliyenseyo, dziko la Malawi ndi dziko la khalidwe chifukwa cha chikhalidwe cha anthu okhala kunoku. Tisamataye mbiri Imeneyo kamba akuti wina akhonza kungotipatsa timaswiti titatu kuti tichite chipongwe, mawa tidzakhala pa mtetete” anatsindika Chakwera.

A Chakwera anafika ku Mangochi atachoka kukatsogolera mwambo opeleka ma satifiketi, ma diploma ndi ma degree kwa ophunzira 344 a ku sukulu ya ukachenjede ya Malawi University of Business and Applied Sciences MUBAS mu mzinda wa Blantyre.

Mawu a Banda anadza pomwe mtsogoleri wakale Bakili Muluzi adamangidwa ndi bungwe lothana ndi ziphuphu ndikatangale mdziko muno la Anti-Corruption Bureau ACB, powanganizira kuti anasokoneza ndalama zoposa $11 million.

A Bakili anali ndi milandu yambiri yoti ayankhepo pomwe adachoka pa mpando wa utsogoleri wa dziko, maka pozembetsa ndalama za chitukuko cha dziko zomwe zinachoka Ku mayiko ena ndipo ati anazilowetsa mmatumba mwawo, milandu yomwe a Muluzi iwo eni adaikana.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading