
Nthambi ya ndende ya Malawi Prison Service yati ophunzira okwana 62 a mndende ndi omwe alemba nawo mayeso a Malawi National Examination Board (MANEB) a standard 8 chaka chino.
Mneneli wa nthambi ya Ndende a Steve Meke ati malo asanu ndi awiri a Ndende olembetsa mayeso ndi omwe osungidwa mndendezi akulembelamo mayeso.
A Meke ati ophunzira 84 amayenera kulemba nawo mayesowa koma ena mwa iwo adamaliza nthawi yawo yokhalira mndende, zomwe zinachepetsa chiwelengelochi.
Iwo ati pambali pa kulimbikitsa maphunziro a ku pulayimale komanso ku sekondale, nthambi ya ndendeyi ikupitiliza kusula ndi kutulutsa ma luso osiyanasiyana ofunikira kwa anthu okhala mndende kuti pamene adzatuluke adzakhale nzika zotha kupanga ziganizo mozindikira.
Ndende za Maula, Mzuzu, Zomba, kachere women, Chichiri ndi Bvumbwe ndi zomwe zatulutsa ophunzira omwe alemba nawo mayeso a Primary School Leaving Certificate of Education PSLCE.
Ophunzira a Standard 8 oposa 200 sauzande adayamba mayeso awo lachitatu ndipo atsilia kulemba mayesowa lero lachisanu.