Dedza Dynamos yazomola mphunzitsi wakale wa Wanderers Alex Ngwira


Ngwira

Timu ya mu ligi yayiku mdziko muno ya Premierbet Dedza Dynamos yadyelera maso ntchito za mphunzitsi wakale wa Mighty Wanderers Alex Ngwira, kulowa m’malo mwa a Andrew Bunya omwe awachotsa ntchito ku timuyi masiku apitawo.

Wachiwiri kwa wapampando ku timu ya Dedza Mavuto Mugode atsimikiza za kufika kwa a Ngwira ku timu ya Dedza ponena kuti akuyembekezera kuti a Ngwira awombola timu yawo pobweletsa zotsatira zolozeka malinga ndi ukadaulo omwe ali nawo.

Potsimikiza za nkhaniyi, a Mugode ati a Ngwira afika kale m’boma la Dedza kukonzekera kukamalizitsa zonse zofunika pa ntchito yawo.

Timu ya Dedza Dynamos masiku anayi apitawo inachotsa ntchito mphunzitsi wake wakale Andrew Bunya ati chifukwa cha kusachita bwino kwa timuyi chiyambileni ligi yayikulu mdziko muno, ya TNM Super League.

Timuyi yomwe ili pa nambala 10 ndi ma point ake asanu ndi imodzi 6, ikuyembekezeka kukumana ndi timu ya Civil service United pa bwalo la Dedza kumathelo a sabatayi.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading