
Bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) ladandaula ndikuchepa kwa anthu omwe akufuna thandizo la ngongole.
Mkulu wa bungweli ku Mponela, Lloyd Nyakamela ndiye wanena izi Lachitatu pamwambo opeleka ngongole ya zipangizo za ulimi ku gulu la Mtanga, Mfumu yaikulu Njombwa ku Kasungu.
Bungwe la NEEF, lapeleka matumba 100 a feteleza, mbewu makilogalamu 500, ndizipangizo zamthilira zodalira dzuwa, zandalama zokwana K30 miliyoni ku gulu la Mtanga, yomwe ipindulire amayi makumi asanu (50).
Ndipo poyankhula, Nyakamela wati cholinga cha ngongoleyi, chofuna kuthetsa njara kudzela mu ulimi wa mthilira chitha kukwanitsidwa ngati pangakhale anthu ochuluka otenga ngongolezi.
“Kwa amene akanachedwabe kusafuna kuchita ulimi wa mthilira, tikuwamema kuti abwere chifukwa alimi omwe ifeyo timafuna akutichepela kwambiri” anatero Nyakamela.
Iye wati pakadali pano zipangizo zilipo kale zongodikira anthu akatenge ngongoleyi, yomwe wati sikumachedwa kutuluka.
Malingana ndi Nyakamela, pangongole ya K30 miliyoni yomwe yapelekedwa dzulo, ikuyenela kupindula ndalama zosachepera K200 miliyoni.
Mtsogoleri wa gulu la Mtanga, Madren Phiri wati ndiwokondwa kuti alandira ngongole yomwe ithandize kukweza ulimi wawo.
Ngakhale anali ndichimwemwechi, Phiri wapempha bungwe la NEEF kuti tiwonjezere zipangizo zina potengera kuti ngongole yapano ipindulira anthu 50 okha poyelekeza ndi 118 omwe ali mu gululi.
Ndipo mmau ake Mfumu yaikulu Njombwa yapempha azimayi omwe alandira ngongoleyi kupewa kuchita ukatchyali pobweza ngongoleyi kuti bungweli lidzathandizeso ena mtsogolomu.