
Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wati chilowele iwo m’boma m’chaka cha 2020, amanga ndipo akumangabe zitukuko zoposa 600 ndipo posachedwa atulutsa mndandanda wa zomangamanga zomwe achita kuti aMalawi aweluze mtunda omwe asuntha mzaka zinayi.
Mtsogoleriyu wati dziko likamayandikira kupita ku masankho kumachuluka bodza. Iwo ati chitukuko cha dziko lathunthu sichimangidwa ndi ulamuliro umodzi, ponena kuti sinzeru kudzitamandira chitukuko pa iwe wekha pomati “zomwe mukumanga ndidayambitsa ndine.”
M’mawu awo ku mwambo okhazikitsa tsiku lokumbukira zomangamanga ku Bingu International Convention Centre (BICC) mu mzinda wa Lilongwe, a Chakwera ati iwo akungochita mbali yawo kuposa iwo amene anali akatswiri pongoika miyala ya maziko a zitukuko mdziko muno koma osamanga.
“Nkhani pa chitukuko si amene wayambitsa kapena wamaliza koma kuti kodi mu nthawi yanu pa nkhani ya zitukuko mwasuntha mtunda wanji?” Anafunsa a Chakwera.
Nduna ya Zomangamanga a Jacob Hara ati kulimbikitsa zomangamanga ndi khumbo lofuna kumanga Malawi okongola, pomwe ati onse ochita katangale pa nkhani ya zomangamanga sakuyenera kupatsidwa mpata.
A Hara ati unduna wawo unafufuta pa mndandanda ma kampani okwana 13 chifukwa cha ukambelembele osiyanasiyana ndipo anati izi nzosaloledwa mu ulamuliro wa a Chakwera.
Apo ndi pomwe a Hara anati dziko muno mukuchitika komanso mwachitika kale zitukuko zoposa zana limodzi.
Tsiku lokumbukira ntchito ya zomangamanga lomwe lakhazikitsidwa lero pa 2O May, lidzikumbukilidwa chaka chilichonse mdziko muno.