Mponda walanda ukaputeni kwa Senaji kupeleka kwa Aaron

Advertisement
Lloyd Aaron

Mphunzitsi wa FCB Nyasa Big Bullets Peter Mponda walanda utsogoleri wa ukaputeni (Captain) mwa Clyde Senaji ndi kupeleka kwa Lloyd Aaron.

Poyamba mphunzitsi Mponda anasankha Senaji ngati Captain koma m’masewelo angapo omwe amatenga utsogoleri pa amzake anali Àaron kapena Frank Willard.

Mponda tsopano wasankhiratu osewera wapakatiyu ndipo omutsatira wake ndi Yankho Singo ndipo ngati awiriwa sanapezeke, udindo udzigwa m’manja mwa osewera akuluakulu monga; Yankho Singo, Frank Willard, Mike Mkwate, Babatunde Adepoju kapena Richard Chimbamba.

Mponda wati kukhala otsogolera osewera amzake munthu (captain) sikungovala chapamkono (armband) kokha, koma zimatengelanso kuti munthu akhalenso mtsogoleri ndithu.

“Tili ndi zifukwa zomwe zatibweletsa ku chiganizochi, Senaji anadziwitsidwa kale masabata atatu apitawo, si nkhani kwa iye, chifukwa iyi ndi nkhani ya m’chipinda mwathu yoti sitingangowuza aliyense koma Senajiyo analandira nkhaniyi bwino bwino,” analetelo Mponda.

M’masewelo a Lachitatu pa bwalo la Dedza pomwe Bullets inaswa Dedza 1-0 pa mphindi ya chi 89, Lloyd Aaron ndiye anavala cha pamkono (Armband) kuti ndiye mtsogoleri wa osewera amzake.

Advertisement