Anamwino tidzilemekeza ntchito yathu – Bertha Kanyinji

Advertisement
Kanyinji

Namwino wapachipatala cha Mchinji, Bertha Kanyinji walimbikitsa a namwino amzake mdziko muno kugwira ntchito modzipeleka komaso kutsatila malamulo a ntchito nthawi zonse panthawi ya ntchito.

Kanyinji wayankhula izi atasankhidwa komaso kukwezedwa udindo ndimtsogoleri wadziko lino, Lazarus Chakwera ngati Namwino yemwe wagwira ntchito mwapamwamba m’boma la Mchinji. 

Pa mwambo okumbukira a namwino pa dziko lonse lapansi omwe unachitika pa 12 May, 2025, pabwalo lazamasewero la Nkhwazi ku Mchinji, mtsogoleri wa dziko linoyu analengeza kuti wakweza udindo a namwino mmaboma ena omwe agwira ntchito motamandika, omwe ndikuphatikiza a Kanyinji komaso bambo Lusungu Mvalo kuchoka ku Mchinji.

“Ichi ndichilimbikitso pa ntchito yanga komaso ndiphunziro kwa a namwino onse kuti tidzilimbikira ntchito. Ndikuthokoza kwambiri mtsogoleri wadziko lino potilimbikitsa motere chifukwa izi sizomwe ndimayembekezera,” anatero Kanyinji. 

Kutsatila kukwezedwa udindoku, a Bertha Kanyinji achoka pa grade J ndipo tsopano afika pa grade I.

Kukwezedwaku ndikwachitatu kamba koti anayambila pa grade K mu dzaka zawo zoyambilira pa ntchito ndipo tsopano afika pa grade I atagwira ntchito kwazaka 23 ngati Namwino.

Advertisement