Wanderers yaswa MAFCO pa Kamuzu, Songwe ikugawabe ma point

Advertisement
TNM Super League

Timu ya Mighty wanderers yagonjetsa timu ya Malawi Armed Forces College MAFCO 2-0 pa bwalo la Kamuzu mu TNM Super League.

Chigoli chomwe chikhonza kukhala cha mwamsanga kwambiri chiyambileni League pa mphindi yachitatu mpira utangoyamba, osewela wakale wa Dedza Clement Nyondo ndi yemwe anapatitsa chitsogozo anyamata a Lali Lubani.

Masewelowa anatenga mphamvu chigoli chitangobwera ndipo kunali phuma la asilikali a MAFCO kufuna kubweza kuti mwina nkukhala pa ndendende koma anyamata a kumbuyo kwa wanderers Cholopi, Sanudi, Chaziya ndi Nyirenda anakana, komanso ma bomba awo amangopita m’mbali mwa golo la Chancy Mtete.

Chigawo choyamba chikunka kumapeto pa 40, Nyondo anabwera ndi kupeleka mpira kwa mzake yemwe anali naye ku Dedza Dynamos, Promise Kamwendo yemwe sanaphonye koma kugwedeza ukonde wa MAFCO 2-0.

M’chigawo chachiwiri mphunzitsi wa Wanderers Bob Mpinganjira anatulutsa Clement Nyondo, Dan Kudomto ndi Francisco Madinga kulowa Blessings Mwalilimo, Felix Zulu ndi Gaddie Chirwa.

Wanderers inapanikiza nthawi yakuthaitha kudzera mwa Gaddie Chirwa, Mpinganjira ndi Mwalilimo komabe zinakanika kubweletsa cholowa.

Pakutha pa zonse oyimbira Zebron Lengani anaweluza kuti Wanderers ndiyo yawola onse pa Kamuzu.

Pomwe pa bwalo la Karonga, Silver Strikers yakapamantha Songwe Boarder United.

Oyimbira Joshua Msiska anaweluza kuti zigoli ziwiri za Festus Duwe, Chimwemwe Idana ndi Emmanuel Allan zikhale zokwana Silver kutenga ma point onse atatu pomwe Songwe yapata cholilira kudzera mwa Wongani Kamanga pa penate.

Pakutha pa zonse masewelo a Songwe ndi Silver Strikers 4-1.

Advertisement