A Gangata ndinawalemberadi mayeso – yavomela mboni ya boma

Advertisement
Gangata

Mboni yoyamba ya boma a Andrew Elia Mphamba apelekera umboni m’bwalo la milandu mu mzinda wa Lilongwe kuti ndi iwo adalembera mayeso wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) mchigawo cha pakati, a Alfred Gangata.

A Mphamba anauza bwalo la milandu lero momwe a Alfred Gangata anawapatsira ntchito yokawalembera mayeso mchaka cha 2017.

Mboniyi yati kufikira pano palibe zomwe iwo anapezako ngakhale kulandira kuchokera kwa a Gangata malinga ndi zomwe analonjezana za dipo lowalembera mayeso a folomu folo.

Mboniyi yomwe ndi yoyamba mwa mboni zisanu nzitatu (8) zomwe aboma abweletse yati, ngakhala mphunzitsi wamkulu pa sukulu ya Chitowo komwe adakalembera mayeso akhonza kutsimikiza ndi kuwazindikira a Mphamba ngati a Alfred Gangata.

Bwaloli layima kaye kufikira pa 27th May Chaka chomwechino, Loya wa mbali yozengedwa a Khwima Mchizi ati adzafunsa mboniyi bwalo likakumananso.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha DPP mchigawo cha pakatiyu anamumanga miyezi yapitayo pa mlandu opezeka ndi satifiketi ya Malawi School Certificate of Education (MSCE) mwachinyengo yomwe anayipeza mzaka za m’ma 2017/2018.

Advertisement