
Timu ya dziko lino ya anyamata ‘The Flames’ yafika mu ulendo wake ochokera mdziko la South Africa komwe inakasewera ndi timu ya dzikolo ya Bafana Bafana Lamulungu.
Malawi yabwera koma itausiya mpikisano wa CHAN pa bwalo la Loftus mdziko la South Africa pomwe inagonja 2-0 ndi 2-1 posonkhetsa zigoli zonse za masewelo awiri.
Osewera a Flames abwera kuchokera mu mzinda wa Pretoria ndipo atela kuno kumudzi kudzera pa bwalo la ndege la Chileka International mu mzinda wa Blantyre.
Atantha masewelo a dzulo, Peter Mponda yemwe ndiothandizira mphunzitsi anati Flames simayenera kugonja ndipo anayesetsa m’maseweledwe koma kuti kumbuyo kwa timuyi nkumene anyamata a Bafana Bafana anakuwonelera.
Mponda anati zinali zotheka kuti masewelowa athere ndi chipambano chochoka pa bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe.