Loto la Flames mu CHAN lafela ku Joweni

Advertisement
Flames

Timu ya dziko lino ya mpira wa miyendo ya amuna ‘The Flames’ yagonja ndi kutuluka mu mpikisano wa CHAN Lamulungu kutsatira kugonja 2-0 ndi Bafana Bafana pa bwalo la Loftus mu mzinda wa Pretoria mdziko la South Africa.

Masomphenya a Malawi okasewela nawo ku ndime yotsiliza ya mpikisano wa CHAN omwe amayitana osewela a mdziko lomwelo basi, anayamba kusuluka pamene South Africa inapeza chigoli chake choyamba pa mphindi ya chi 12 kudzera mwa osewelanso kutsogolo mu timu ya TS Galaxy Vitor Letsoalo kuyika zigoli pa 1-0 ndi 1-1 posonkhanitsa zonse

Pasuwa yemwe lero sanapezeke pa bwalo la Loftus Versfeld chifukwa cha kudwala, anadalira koyamba anyamata monga, George Chikooka pa golo, Macdonald Lameck, Maxwell Paipi, Lloyd Àaron, Nickson Mwase, Yankho Singo, Binwell Katinji, Alick Lungu, Wisdom Mpinganjira, Promise Kamwendo ndi Wongani Lungu.

Ngakhale imatsalira m’masewelo koma Flames inali ndi ukalibe kufuna chipambano, koma timu ya Molefi Nsteki inali kugogoda nayo kudzera mwa Neo Maema, Siyanda Nsani, Kamogelo Sebelele ndi Victor Letsoalo omwe anapeleka ntchito yolemetsa kwa anyamata otchinga kumbuyo kuphatika goloboyi Chikooka.

Pomwe mphindi zimapita kosendera masewelo ali pa 1-1 kuti mwina masewelo nkupita ku mphindi 30 zina kapena ma penate kumene, pa 87 anabwera captain wa Bafana B’ Neo Maema yemwe anasakaza zinthu za Pasuwa ndipo masewelo anathela 2-0 (2-1 pa aggregate)

Timu ya South Africa inabweletsa osewera achilendo okwana asanu ndi m’modzi (6) omwe m’masewelo oyamba sanapezeke.

Malawi imapita mu masewelo a lero koma ikutsogola kale 1-0 chipambano chomwe inapeza m’maswelo oyamba pa bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe, ndipo chipambano cha South Africa chagula malo mu ndi ndime yotsiliza ya 2024 African Nations Championship (CHAN), masewelo omwe akachitikira ku Tanzania, Kenya ndi Uganda kuyambira pa 2 mpaka pa 30 August 2025.

Advertisement