
Timu ya dziko lino ya mpira wamiyendo ya ‘The Flames’ yafika mu mzinda wa Pretoria m’dziko la South Africa kukonzekera kubwerezana ndi timu ya dzikolo ya Bafana Bafana Lamulungu lino mu masewelo a mu mpikisano wa CHAN.
Flames yanyamuka lero ku m’mawaku kudzera pa bwalo la ndege la Kamuzu mu mzinda wa Lilongwe ndi osewera 21.
Malawi ikupita pa bwalo la Loftus Lamulungu lino koma ikutsogola kale 1-0 chigoli chomwe chinabwera m’masewelo oyamba pa bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe kudzera kwa Zeliat Nkhoma pa mphindi ya chi 87. M’masewelo a Lamungu Malawi idzangofunika kufananitsa mphamvu kapena kupambana kuti ipitilire
Mphunzitsi wa Flames Kalisto Pasuwa anauza atolankhani asananyamuke kuti iwo sakupita kuti akangotchinjiriza chigoli chomwe anapeza koma kukalimbikira kupambana potengera kuti nayo Bafana Bafana ndi timu yabwino.
Pasuwa wati nkhondo inangoyamba pa Bingu ndipo kwatsala ndi kumalizitsa posatengeka ndi chipambano cha m’masewelo oyamba.
Zadziwika kuti mphunzitsi wa South Africa Molefi Ntseki wawonjezera anyamata ake okwana asanu ndi m’modzi omwe masewelo oyamba sanawoneke chifukwa pa tsikulo kunalinso masewelo a mphamvu a SOWETO Derby pakati pa Kaizer Chiefs ndi Orlando Pirates.
Koma osewera onse amene watenga Pasuwa mndandanda uli motele;
GOALKEEPERS
Richard Chimbamba
George Chikooka
DEFENDERS
Macdonald Lameck
Nixon Mwase
Maxwell Paipi
Emmanuel Nyirenda
Andrew Jovinala
Alick Lungu
MIDFIELDERS
Yankho Singo
Lloyd Aaron
Chawanangwa Gumbo
Wongani Lungu
Charles Nkhoma
Blessings Singini
ATTACKERS
Zeliat Nkhoma
Olson Kanjira
Binwell Katinji
Wisdom Mpinganjira
Gaddie Chirwa
Promise Kamwendo
Chikumbutso Salima.