Milandu ya Phwedo inalowanso m’bwalo lero, oweluza wayimitsa kaye

Advertisement
Phwedo

Milandu iwiri ya katswiri ochita zisudzo Tumpe Mtaya yemwe amadziwika ndi dzina loti “Phwedo” inalowanso m’bwalo la milandu la Lilongwe Principal Resident Magistrate kuti katswiriyu apitilire kuyankhapo.

Phwedo lero Wakana pamaso pa bwalo milandu yake yonse iwiri; ogonana ndi mwana osakwana zaka 18 komanso mlandu wina ozembetsa mwana, yomwe a mbali ya boma anamumanga nayo.

Oweluza milandu Principal Resident Magistrate, Benjamin Chulu wayimitsa kumva milandu ya katswiri “Mtaya” mpaka pa 16 May pomwe adzagamule zokhudza pempho la mbali yozengedwa lomwe ati akufuna ambali ya boma awapatse zikalata za umboni za zomwe ma dotolo anagwiritsa ntchito poyeza zaka za mwana oganizilidwayu komanso kuti awapatse chiphaso chake cholembera mayeso a folomu folo.

Pa nthawi yomva milanduyi oyimira milandu wa Phwedo a Khwima Mchizi anapempha mbali ya boma kuti ipeleke ma umboni ogwirika kuti Mtaya athe kuyankhapo bwino.

A Mchizi anapemphanso bwalo kuti mbali ya boma iwapatse chiphaso (ID) cha mwana oganizilidwayu chomwe anagwiritsa ntchito polemba mayenso ake Malawi School Certificate of Education (MSCE) chaka chatha.

A Mchizi anafunsanso bwalo kuti aboma awapatse zikalata zokwana zogwirika zokhudza lipoti lomwe boma linabweletsera poyera poyeza zaka za mwanayu komanso zithunzi zomwe dotolo anajambula poyeza zaka za mwanayu.

Loyayu wati akufuna izi cholinga choti zotsatilazi, nayo mbali yawo athe kuzipititsa kwa ma dotolo ena otsata kuyeza zaka kuti akwanitse kuyimila ndi kuyankhapo pa ma umboni a mbali ya boma.

Mbali ya boma pomwe imayankha inati potengera kuti oganizilidwayu wakana milanduyi ndi udindo wawo kubweletsa umboni tsopano kuwonetsa kuti a Mtaya anapalamuladi.

Apo ndi pomwe oweluza Chulu anayimitsa kaye milanduyi.

Milandu ya Phwedo ikupitiliza kukoka chidwi cha anthu ochuluka omwe amamutsatira kuti amve mathero a milandu yake, potengera kuti ena samakhulupilira kuti milanduyi ndi yowonadi kapena ikufanizidwa ndi zomwe zili mu kanema wa ‘Welcome to Maula’ yemwenso muli  Phwedo.

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.