
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Michael Usi ati nthawi zina zimadabwitsa kuti atsogoleli ena a mipingo amakhala ngati ntchito yomwe ilipo ndi yongodzudzula andale kuposa kuwathandiza anthu kukalowa kumwamba.
Poyankhula pa mwambo wa maliro a Chikumbutso Mtumodzi ku Chankhungu m’boma la Dowa lero, a Usi ati ndale zili potelopo, koma atsogoleri a mipingo pomwe akudzudzula andale, asamayiwale chofunika cha dziko.
“Mulungu amafuna anthu abwino kuti tonse tikalowe kumwamba, pempho langa ndi lonena kuti, ndale ndi zimenezo, zitidzudzulani mukatipeza m’mene m’matidzudzulira muja komano musamaiwalenso ntchito yanu yonena kuti muyang’ane chofunika cha dziko kuwakonzekeretsa anthu kukalowa kumwamba.
“Chifukwa nthawi zina zimadabwitsa kukhala ngati kuti nthawi zonse ampingo ntchito imene ilipo ndi yonena za ndale zokhazokha ndikukulankhulani monga inu odzozedwa,” anatero a Usi.
Iwo anatinso m’chitidwe ochitilana nsanje ndi kuyipa mtima pa ena zakula modabwitsa mdziko muno pomwe ati ngakhale munthu kungolembedwa ntchito kumene, anthu amakuda.
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dzikoyu wadandaulira a mipingo kuti alimbikitse kubweretsa chikondi pa aMalawi.
A Usi anawonjezera kuti pali anthu ena omwe akuwona kuti zitukuko zomwe akupanga a boma lomwe lilipo pano sizoyenera, ndipo akumasankha kuziwononga ndi cholinga choti awoneke kuti sakupanga kanthu.
A Usi anakayimilira mtsogoleri wa dziko lino pa mwambo wopelekeza thupi la a Chikumbutso Mtumodzi omwe anamwalira Lolemba pa chipatala cha Partiners in Health mu mzinda wa Lilongwe.
A Mtumodzi asadamwalire adakhalapo m’neneli wa mtsogoleri wa dziko lino malemu Bingu wa Mutharika ndi a Joyce Banda, komanso adagwirapo ngati wamkulu wa nthambi ya mauthenga ndipo pa nthawi yomwe amamwalira anali mlembi wamkulu ku nthambi yogula katundu ku boma.