
Katswiri pa ndale George Phiri wati aphungu a Nyumba ya Malamulo ena, asatangwanike ndi kuwasangalatsa anthu akwawo ndi zinthu lero pomwe mu zaka zisanu zonse zomwe zapitazi akhala akudya okha, pomwe atsindika kuti anthu akwawowo pano anazindikira kuti ‘inuyo si munthu oyenera.’
A Phiri ati pa zaka zonse aphungu ena kufikira lero alibe choti akhonza kuloza chomwe awachitira anthu a ku dera la kwawo, ndipo kuyima nkumafunanso voti ya anthuwa ndi kungodzikonda chabe komanso dyera.
Polankhula mu pologamu ya “Pressing issues” pa wailesi ya Kasupe, a Phiri ati anthu m’maderamu palibe chomwe anthu chingawasangalatse kuponyeranso voti munthu amene sanawasangalatse ndipo anawakhumudwitsa.
“Mu zaka zisanu zonsezi amene wadya ndi inuyo, anthu akwanu simunawagawireko, anthu akwanu kulibe chimene akhonza kuloza chimene mwachita, anthu akwanu palibe chimene mukhonza kuloza chimene chingawasangalatse nde mufuna muwasangalatse lero lokha?, dziwani kuti nawonso pano azindikira kuti inuyo si munthu oyenera,” anatelo a Phiri.
Iwo anatsindikanso kuti kuwabweletsera anthu ka jumbo sikusintha kanthu chifukwa anthu azindikira ndipo voti imene ili ku dera limenelo anthu akaponyera wina.
Katswiri wina George Chaima mu pologamu ya “The Brief” wati nthawi yakwana kuti aMalawi agwiritse ntchito ubongo wawo mozama kupewa kusinthitsidwa chiganizo chifukwa cha zinthu zongolandira.
A Chaima ati nzosabisa kuti atsogoleli ena ndi ongokoma mkamwa ndipo aMalawi akuyenera akhale ndi philikanilo lotha kumva ndi kudziwa kuti uyu ndi Psyipsyinthi (wabodza).
A Malawi atsala ndi nthawi yochepa chabe kuti akaponye voti yosankha phungu, ma Khansala ndi mtsogoleri wa dziko pa 16 September chaka chino ndipo bungwe loyendetsa chisankho la MEC, mwezi wa July likhale likutsekulira nyengo yokopa anthu.
Malamu oyendetsera zipani komanso okhudza masankho, opikisana nawo sakuyenera kupeleka zinthu kwa anthu powakopa kuti adzawasankhe, malamulowa akutsindika kuti opikisana akuyenera kugwiritsa ntchito mbalume (mfundo) zokhazokha pokopa mowasankha.