Thupi la Martin Chiwanda lalowa m’manda

Advertisement
Martin Chiwanda

Thupi la Mtolankhani odziwika bwino, Martin Chiwanda, aliyika m’manda lero m’mudzi mwa Kalonga, mfumu yaikulu Ntonda m’boma la Mangochi.

Pa nthawi ya imfa yake, Chiwanda amagwira ntchito ngati mkulu ofalitsa nkhani ku khonsolo ya boma la Machinga.

Malemu Chiwanda anamwalira Lachisanu, pa 2 May, 2025 pa chipatala chachikulu cha boma la Machinga atadwala kwa kanthawi kochepa. Iwowa anali ndi zaka 41.

Poyankhula pa mwambo operekeza malemuwa, m’modzi mwa akubanja, Lucius Msosa anati ndi okhumudwa ndi imfa ya m’bale wawoyu chifukwa anali msanamira yawo.

“Ife akubanja ndife achisono kwambiri chifukwa malemuwa anali potsamira pathu ndipo amatipatsa nzeru komanso thandizo mu njira zambiri,” anatero a Msosa.

Ndipo m’mawu ake, wachiwiri kwa mkulu ya nthambi yofalitsa nkhani mu unduna wa zofalitsa nkhani, Lissah Malango, anati undunawu wataya munthu odzipereka pa ntchito yake.

“Ndife osweka mtima chifukwa cha imfa ya nzathu Martin, makamaka powona kuti imfa yake yadza pa tsiku lomwe atolankhani padziko lonse amakondwelera tsiku lawo,” anafotokoza a Malango.

Malemu Chiwanda asiya mkazi ndi ana awiri.

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.