
Nduna ya zofalitsa nkhani, Moses Kunkuyu yemweso ndi m’neneri wa boma, wakanitsitsa mwantu wagalu kuti iye adanena kuti boma lidasunga black box ya ndege yomwe idapha Saulos Chilima ndi ena asanu ndi atatu chaka chatha.
Izi zikubwera pomwe chichitikireni ngoziyi anthu akhala akuloza chala Kunkuyu kuti adanena kuti black box idasungidwa ndi boma, zomwe nzosemphana ndi lipoti la ngoziyi lomwe lidati ndegeyi idalibe black box, kupangitsa anthu kukhalebe ndi mafuso osayankhidwa ochuluka.
Koma poyankhula ndi wayilesi ya Times kumathero a sabata yapitayi, Kunkuyu watemetsa nkhwangwa pa mwala kuti pakamwa pake sipadaneneko kuti boma lasunga black box yomwe imatepa ndikusunga zochitika zonse ndege isadachite ngozi.
Poti kutsutsa galu nkukumba, Kunkuyu wapempha nyumba zofalitsa nkhani m’dziko muno kuti ziwulutse pologalamu yomwe iye adatepedwa akuyankhula kuti black box yasungidwa ndi boma.
“Tatengani ma recording amene aja, inuyo osati ife, musewere chimodzi chimodzi kuti zimene zidayankhulidwa nthawi yonse yangozi ija ndi izi, mupapeze pamene padayankhulidwa chichewa chimenecho, simupapeza.
“Nsonkhano wa atolankhani uli onse omwe udachitika, mukapita lero pa internet mukaupeza. Kodi bwanji inuyo (ma wayilesi) osalithandiza dziko la malawi kubweretsaso ma interview amenewa, chingakuvuteni nchiyani?” watelo Kunkuyu.
Iye wati chomwe akukumbukira kuti adayankhula ndi chakuti adanena kuti ndege ili yose ikamagulidwa imakhala ndi zizindikiro zake (standard features) komaso kuti pamakhala zinthu zina zimene mumatha kukaikitsa kuti zikhalemo.
Atafusidwa ngati ndege yomwe idachita ngoziyi idalidi ndi black box kapena ayi, Kunkuyu adati iye siwoyenera kuyankha funso limenelo koma akuluakulu a Malawi Defense Force.
“Nde fuso nkumati kodi black box ndi standard feature? Nde ngati ayikilira chinthu china amakalemba m’buku lake lija nde zimenezo angayankhe ndi eni ake a ndege a MDF,” adatelo Kunkuyu.
Ngozi ya ndegeyi idachitika pa 10 June, 2024 pomwe Chilima yemwe adali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino komaso ena omupelekeza ankapita ku maliro a Ralph Kasambara ku Nkhatabay.