
Sukulu yaukachenjede ya Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (LUANAR) yachenjeza aphunzitsi komaso ophunzira ake kuti asati maso bilubilu pa chamba chomwe sukuluyi ikulima ponena kuti nchopanda ukali.
Malingana ndi uthenga omwe sukuluyi yatulutsa, chambachi chomwe chikulimidwa ku Bunda Campus chili ndi 3% ya ukali (Tetrahydrocannabinol – THC) yomwe ndiyotsika kwambiri ndipo yati obanda chamba ngati chimenechi sangafile ayire.
Sukuluyi yachenjeza ophunzira onse pa sukuluyi omwe anachayilira kuti masiku amenewa azipeza mogo mosavuta komaso mwaulelere pomakaba m’munda wa sukuluwu, kuti opezekayo awonetsedwa mbonawona.
Sukuluyi yatsindika kuti chambachi ndichongopangira malisechi pansi pa Africa Center of Excellence in Aquaculture and Fisheries (AquaFish).
Malingana ndi tsamba la Leafwell, chamba chokhala ndi 15% ya THC kapena kupitilira apo, ndi chomwe chimapangitsa wosuta kuyamba kuwona anthu chozondoka.