
Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wati Papa Francis anali odabwitsa machitidwe ake ponena kuti anali odzichepetsa komanso wa umunthu ngati munthu wamba.
Poyankhula pomwe anapemphera nawo pa mwambo opemphelera mzimu wa Papa Francis ku Maula Parish mu mzinda wa Lilongwe, a Chakwera ati mu nthawi yomwe iwo anakhala mu nyengo zowawa za utsogoleri wawo m’dziko lino, Papa Francis anawonetsa chikondi ndi umunthu polimbikitsa ndi kuthunzitsa mitima ya aMalawi chifukwa cha nyengo zowawa zomwe dziko lino limadutsamo.
A Chakwera ati Papa anali okonda kupemphera, kulimbikitsa ena, wa umunthu, olimba mtima, othandiza ovutika, okhulupilira, okonda kupemphera ndi okhala ku mbali ya aliyense mosatenga mbali ndipo Papa Francis anawonetsa kupemphera nthawi zonse za moyo wake.
Archbishop George Desmond Tambala wa Archdiocese ya Lilongwe wayamika mapemphero opemphelera Papa Francis omwe achitika mu ma parish okwana 49 m’maboma angapo a pansi pa diocese ya Lilongwe.
Poyankhula pa mwambowu Tambala wapempha akhristu a mpingowu kuti apitilize kupemphelera mzimu wa Papa Francis yemwe walowa m’manda lero.
A Tambala ati Papa Francis anali ndi chidwi kuti anthu ambiri amudziwe Yesu mkhristu, ndipo anayesetsa kuti mayiko a nkhondo mubwelere mtendere.
Akhritu ambiri a mpingo wa Katolika lero achita mapemphero opemphelera mzimu wa Papa Francis yemwe anamwalira lolemba ku Vatican ku Rome ndipo wayikidwa lero mu kachisi wa St Mary’s Major Basilica omwe ndi Kachisi wa zaka pafupifupi 1,600 omwenso Papa Francis amakonda kupempheramo asananyamuke ulendo uliwonse.
Papa Francis anakhala Papa kwa zaka 12 pomwe anakhazikitsidwa mchaka cha 2013, iye ndi Papa wa chi nambala 8 kuyikidwa panja pa Vatican mu St Mary’s Major Basilica.