Ndilibe mantha ndi aliyense – Zulu 

Advertisement
Zulu

Mphungu wakumadzulo kwa mzinda wa Lilongwe, George Zulu wati alibe mantha ndi aliyense patsogolo pazisankho zachipulura za chipani cha Kongeresi.

Zulu amayankhula izi kutsatila zipolowe zomwe zinachitika pakati paotsatila Kongeresi, omwe akuganiziridwa kuti ndi otsatila ake komanso yemwe akufuna kupikisana naye dela la Mtandire Mtsiriza, Ruth Chingwalu.

Koma poyankhapo pa nkhaniyi, Zulu watsutsa kuti zipolowezi zinakhudza otsatila ake ponena kuti izi zimachitika anthu ake atachokako kale ku likulu lachigawo chapakati la Kongeresi komwe kunali mpungwepungwe-wu.

“Ine ndi onditsatila tinapitadi ku likulu la MCP mchigawo chapakati komwe amakandivomeleza kuti ndiyimile pazisankho zachipulura ndipo tinachokako popanda chisokonezo chilichonse”

“Koma ndinamvetsedwa kuti litafika gulu la Ruth Chingwalu, linayamba kumenya adindo a dera pa phungu (constituency) ndipo anthuwa anayimba lamya kuyitana amzawo kuti akawapulumutse” anatero Zulu.

Dzulo, otsatila Ruth Chingwalu anadandaula kuti Zulu mogwirizana ndi adindo ena ku likulu la chigawo chapakati mchipanichi akuwakhomelera powopa kuti adzapambana, zomwe George Zulu watsutsa kuti alibe mantha ndi aliyense.

“Ine sindingawope kupikisana ndi munthu ngati amene uja. Choyamba dziwani kuti sabata yatha anakadzipeleka ku UTM kenaka zavuta kumeneko wapita ku DPP, ndie ine sindingawope kupikisana ndi munthu yemwe sakupanga za MCP”.

“Mutawafusa, nsalu za MCP ayamba kuvala dzana, koma ine sindingawope munthu olo atati abwere leroli sangaphule kanthu ndipo ine pa 16 September pano ndidzayimira MCP pa zisankho”.

Mmau ake mneneri wa MCP, Jessie Kabwira, anapempha kuti timupatse mpata okwanira kuti afufuze kaye asanayike mulomo pa nkhaniyi.

Pakadali pano sizikudziwikabe tsogolo la Ruth Chingwalu lopikisana nawo pa zisankho zachipulura.

Likulu la chigawo chapakati la Kongeresi likuyembekezeka kuwulura tsiku lomwe zisankho zachipulura zichitike ku Mtandire komaso Mtsiriza koma kwagawidwa posachedwapa ngati dera la phungu wa nyumba yamalamulo kuchoka ku dera la kumadzulo kwa Mzinda wa Lilongwe.

Advertisement