Khonsolo ya mzinda wa Lilongwe ipereka chilolezo ku chipani cha DPP

Advertisement
DPP Rally

Khonsolo ya mzinda wa Lilongwe yapereka chilolezo ku chipani cha Democratic Progressive (DPP) kuti chipanichi tsopano chitha kuchititsa misonkhano yoyimayima m’madera ena a mu mzinda-wu.

Izitu zikudza pamene pangodutsa nthawi yochepa khonsoloyi itakana pempho la chipani cha DPP ati kaamba kakuti nthawi yokopa anthu siidakwane.

Chaima
Chaima: Zipani zonse zizipatsidwa danga lopangitsa misonkhano mofanana.

Mu chikalata chomwe walemba mkulu wa khonsoloyi, Dr. Macloud Kadam’manja, khonsoloyi yati chipani cha DPP tsopano chitha kuchititsa misonkhano m’madera monga; Chilinde, Kawale komanso Biwi, Loweluka lino pa 12 April, 2025.

Pothilirapo ndemanga pa nkhaniyi, katswiri pa nkhani za ndale, Dr. George Chaima, wati anali odabwa ndi chiganizo chomwe khonsoloyi inapanga pokaniza chipani cha DPP kuchititsa misonkhanoyi ponena kuti atsogoleri a zipani zina zandale nawo akuchititsa misonkhano yonga yomweyi ndipo sanakanizidwepo chilolezo.

“Ndi zoona kuti nyengo yokopa anthu siidakwane. Komabe, ndi zodabwitsa kuti atsogoleri a zipani zina za ndale akupatsidwa mpata ochita misonkhano yokopa anthu ngati yomweyi ndipo sanakanizidwepo chilolezo monga momwe zinakhalira ndi chipani cha DPP,” anafotokoza a Chaima.

A Chaima ati ndi kofunika kuti adindo azipereka mwayi ofanana ku zipani zonse molingana ndi malamulo a dziko lino komanso mfundo za ulamuliro wa demokalase.

Advertisement