Anandithamangitsa mu chipani cha UTM – Usi

Advertisement
Dalitso-Kabambe-Michael-Usi

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Michael Usi ati iwo sanachoke mu chipani cha UTM koma anangothamangitsidwa.

“Ndati ndikonze malo amodzi. Ku UTM sinachokeko koma anangondithamangitsako ndipo anthu ache ali pompano. Sikuti ndikudana nawo ayi, koma chilungamo chidzidziwika,” anafotokoza a Usi.

Iwo anatsindikanso: “Ndimati ndikonze chifukwa anthu mumalemba kuti ayi anachokako koma ine ndinathamangitsidwa.”

A Usi amayankhula izi ku Phalombe pa mwambo wa maliro a malemu Alex Joseph Mulli, omwe anali m’chimwene wa a Leston Mulli, mkulu wa kampani ya Mulli Brothers Holdings Limited (MBL).

Iwo amathilira ndemanga pa ulaliki omwe m’busa Billy Gama wa mpingo wa CCAP analalikira pa mwambowu.Mu ulaliki wake, m’busa Gama anadzudzula mchitidwe wa anthu andale m’dziko muno omwe akuti amakondana mwachiphamaso chabe.

A Usi anati iwo alibe mdani pa ndale ngakhale m’modzi.

“Palibe munthu aliyense wandale olo ku UTM ndimati ndikamagona ndimamufunira zoipa,” anatero a Usi.

A Usi anakumana koyamba pa gulu ndi mtsogoleri wa chipani cha UTM, Dalitso Kabambe, chiwachotseleni mchipanichi mu mwezi wa December chaka chatha.

Chipani cha UTM chidalengeza kuti chidachotsa a Usi mchipanichi ati pa zifukwa monga zofuna kugawanitsa chipanichi komanso kusapota utsogoleri wachipani cha Malawi Congress (MCP).

A Usi anakhalapo wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha UTM ndipo atamwalira mtsogoleri wa chipanichi a Saulos Klaus Chilima mu June chaka chatha, a Usi analowa m’malo mwa a Chilima ngati mtsogoleri wongogwilizira wa chipanichi.

Advertisement